Chichewa Christian Hymns
Hymn 488 M’MANJA a Yesu wanga
M’MANJA a Yesu wanga
Ndilikugonamo,
Mommo aphimba ine
Nacho chikondicho.
Mvera! Mudzera m’Mwamba
Mawu a Yesu wanga:
“Mwana, ndidzakusunga
Pano pamtima panga,”
M’manja a Yesu wanga
Ndilikugonamo,
Mommo aphimba ine
Nacho chikondicho.
M’manja a Yesu wanga
Nkhaŵa zonsezo zi!
Momwe zoipa zanga
Sizindibvuta ’yi
Mmomo mulibe nsoni,
Mommo mokoma monse
Sindiliramo msozi,
Ndikondwa m’mtima monse.
Mtima umabisala
M’manja mwa Yesumu;
Mbuye, musunge ine,
Munandifera ’ne.
Ndilinda mopirira
Mpaka wochoka mdima.
Ndikaonana naye
Yesu Ambuye wanga.
