Chichewa Christian Hymns
Hymn 473 YESU wa Kumwamba,
YESU wa Kumwamba,
Mutimvere ife;
Tikugwadirani,
Mwana wa Mulungu.
Ndinu wakuyera
Mfumu yakumveka;
Ife sit’yenera,
Koma mutimvere.
Ndife akuchoka,
Mwina tisokera;
M’njira ya Kumwamba
Mutitsogolere
Mutiletse, Mbuye,
Lero tisachimwe;
Tikondane ndinu
Mutitsuke m’mtima.
Mukatiitana
Tikakhale kwanu,
Tidzayankha, “Mbuye,
Tsopano tili pano.”
(Yesu, Yesu,
Tikugwadirani
Mwana wa Mulungu!)
