Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 466 OSANATU, osana,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 466 OSANATU, osana,

 

OSANATU, osana,
’Naimba anawo;
M’kachisi wa Mulungu
Mwamveka nyimboyo.
’Nalemekeza Yesuyo
Wak’ŵadalitsayo;
Anamuyamikira
M’ubwana wawowo.

Kuphiri la ’Zitona,
Mumpingo wa ’nthuwo,
’namkupizira mnjedza
Naimba nyimboyo,
Angelo akumwambako
Napokerezanso:
“Osana m’Mwambamwamba
Kwa Mlungu wathuyo.”

Zitsamba zakuyera
’Naponya pansipo;
Kukondwa kunamveka
Paphiri ponsepo.
Ambuye yemwe Mfumutu
Nakwera cheteko;
Tiana toyamika
Sanatinyozato.

“Osana m’Mwambamwamba!”
Nyimboyi t’imbenso,
Pokhala Kristu Mfumu
Ndi Mpulumutsiyo.
Timtamandire Iyeyu
Ndi mtima wonsewo;
Tipite kwawo komwe
Tikaimbirenso.

Exit mobile version