Chichewa Christian Hymns
Hymn 464 AKAZI anadza kwa Yesu ndi anawo,
AKAZI anadza kwa Yesu ndi anawo,
Anaŵaletsa anyamata nawakana ndithu;
Ambuye naŵapezadi,
Anati: “Musatero ’yi
Lolani ana abwere kwa Ine,
Lolani ana abwere kwa Ine.
“Ndidzaŵalandira, k’ŵasunga
M’manja mwanga;
Ndi Mbusa wao Inetu, msachotse ana anga;
Akandipatsa mtimawo,
Adzanka ndine Kwathuko;
Lolani ana abwere kwa Ine,
Lolani ana abwere kwa Ine.”
Wokoma Mbuyathu kwitana ana onse;
Atsalanso ambiri ena sanamvera zake;
Sanamva mawu akewo,
Sadziŵa kuti ’natinso:
“Lolani ana abwere kwa Ine,
Lolani ana abwere kwa Ine.”
Afike masiku akuti anthu onse
Adzamva mawu anu ndi kutsata Inu nokha;
Muwale m’mtima mwawomo,
Adziŵe muŵakondanso;
Kopani anthu abwere kwa Inu.
