Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 434 CHIKONDI cha Mulunguyo,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 434 CHIKONDI cha Mulunguyo,

 

CHIKONDI cha Mulunguyo,
Polenga tonsefe;
Analenga awiri,
Mwamuna ndi mkaziyo
Anakhala m’munda mwa Edeni,
Nakondana koposa.

Mulungu anadalitsa,
Banja la awiri;
La Adamu ndi Hava,
Nakondana koposa.
Nalamulira zonse m’mundamo,
Nakondwera koposa.

Analemekeza Mlungu,
Anadalitsika;
Anakhala chitsanzo,
Chachikulu kwa ana.
Nayenda ndi Mlungu nthawi zonse,
Nakondwera koposa.

Exit mobile version