Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 425 AKRISTU ndi abale, tiziyenderana tonse,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 425 AKRISTU ndi abale, tiziyenderana tonse,

AKRISTU ndi abale, tiziyenderana tonse,
Mulungu mmodzi tili naye, ndi Ambuye yemwe,
Chitsime chomwe, njira yomwe yokhulupirira;
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi tiziyenderana.

Atate yemwe anatuma,
Mpulumutsi mmodzi
Kudzatifera kuti atiyanjanitse tonse,
Ndi Mzimu yemwe ayeretsa akumvera onse;
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi tiziyenderana.

Anatipatsa Mawu omwe olimbitsa mtima;
Kumwamba komwe tinka ndi kulonda njira yomwe.
Tibalalikiranji ife akutsata Yesu?
Tiyeni tonse, mMpingo ’modzi tiziyenderana.

Satana apambana tikayamba kusiyana;
Tikayanjana, yemwe adzagonja ndi kuthaŵa;
Mbuyathu adzamthyola konse ndi kumlamulira.
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi tiziyenderana.

Tiphatikane tonsefe okonda Yesu Kristu;
Tisalekane pakugwira ntchito za Mbuyathu;
Tilimbitsane pakuyenda m’njira yonka kwathu.
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi tiziyenderana.

Exit mobile version