Chichewa Christian Hymns
Hymn 418 UDINDO wolalikira Uthenga,
UDINDO wolalikira Uthenga,
Unapatsidwa kwa Yesaya;
Anamva mawu ochoka M’mwamba,
Kutitu ndidzatuma yani?
Anati: “Ndili pano Ambuye,”
Anatulutsa dzanja lake:
Nakhudza pakamwa pa Yesaya,
Namulonga kukhala mneneri.
Limba mtima mbale wanga,
Ndikutuma kudziko lonse;
Upasule, ukagwetse,
Umange kenanso ubzale.
Udindo wolalikira Uthenga,
Unapatsidwatu kwa Mose:
Anamva Mawu ochoka M’mwamba:
“Vula nsapato zako Mose.
Ntchito yomwe ndakuyitanira,
Sintchitotu ya masewera;
Yofunika ukonze mtimawo,
Ukatulutse Ayisrayeli.”
Udindo wolalikira Uthenga,
Unapatsidwatu kwa ife;
Tinamva Mawu a Mbuye Yesu,
Kutitu tikalalikire:
“Mphamvutu zapatsidwa kwa Ine,
Kumwamba ndiponso pansipa;
Ine ndili pamodzi ndi inu,
Kufikira chimaliziro.”
