Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 384 USIKU uja kalero,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 384 USIKU uja kalero,

 

USIKU uja kalero,
Anam’pereka Yesuyo,
Usiku womwe m’manja mbuu!
‘Natenga mkate Iyeyo,

Atayamika Mlunguyo,
Wolamulira pansipa;
Natema mkate natítu,
Kwa omwe anatsatawo.

“Ndi thupi lopatsidwali,
La Ine m’tenge, mudyetu;
Muchite ichi nonse ‘nu,
Ndi chikumbutso changatu.”

Ndiponso m’manja chikhocho,
‘Nakweza, natamandamo;
Mulungu, mtima wake myaa,
Nanena mawu omwewa:

“Chikho cha mwazi wangachi,
Chitsuka mtima woda bii;
Chamapangano omwewo.
Chisomo cha Kumwambako.”

“Chikondi chili m’chikhomu,
Chodzala, ‘mwani nonsenu;
Chipitilire konseko.
Ndi chikumbutso changacho.

Exit mobile version