Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 383 KASUPE ali wodzaza

Chichewa Christian Hymns

Hymn 383 KASUPE ali wodzaza

 

KASUPE ali wodzaza
Ndi mwazi wa Yesu;
Omwe asamba mwa uyu

Ataya zoipa.
Ataya zoipa,
Ataya zoipa;
Omwe asamba mwa uyu
Ataya zoipa.

Woba wakufa ’napenya
Kasupe, nakondwa,
Ndimo inenso mwa uyu
Ndisamba ndiyera.

Ndisamba ndiyera,
Ndisamba ndiyera;
Ndimo inenso mwa uyu
Ndisamba ndiyera.

Mwazi wa Yesu wokondwa
Ukhala wamphamvu
Kwa ana onse a Mlungu,
Uchita kwombola.

Uchita kwombola
Uchita kwombola;
Kwa ana onse a Mlungu
Uchita kwombola.

M’mene ndapenya mwazi wa
Mabala anuwo,
Kukonda kwathu nditama
Kwakutha kwa moyo.

Kwakutha kwa moyo,
Kwakutha kwa moyo;
Kukonda kwanu nditama
Kwakutha kwa moyo.

Kumwamba ndikaimbanso
Zimphamvu za Mlungu,
Zopulumutsa onsewa
Omvana ndi Yesu.

Omvana ndi Yesu,
Omvana ndi Yesu;
Zopulumutsa onsewa
Omvana ndi Yesu.

Exit mobile version