Chichewa Christian Hymns
Hymn 360 KRISTU wakuyeratu,
KRISTU wakuyeratu,
Kristu wakuŵalayo,
Wolungama mdzuketu,
Muingitse mdimawo.
Dzuŵa lathu m’Mwambamo
M’wale m’kati m’mtimamo.
Konse kuli mdima bii
Kosakhala Inutu;
Nlosakondwa tsikuli
Mosaŵala Inu ’mu.
Ndionetu m’katimo
Mwakuŵala kwanuko.
Mudze, mloŵe m’mtimamu,
Mchotse monse mdima bii;
Mdzaze ndi kuyeraku,
Mchotse zosamverazi;
Ndi kuyera kwanuku
Ndikaone bwinotu.
