Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 343 ZOKOMA ndithu nthaŵizi

Chichewa Christian Hymns

Hymn 343 ZOKOMA ndithu nthaŵizi

 

ZOKOMA ndithu nthaŵizi
Kwa Mlungu zondifitsadi;
Kumpando wachifumuwo
Ndiuza zanga zonsezo.
Pobvuta ine mtimamo
Nditulapo pa Yesuyo;
Pakuyesedwa ndinkatu
Kwa Mbuye, sindikhala duu.
Pakuyesedwa ndinkatu
Kwa Mbuye, sindikhala duu.

Zokoma inde nthaŵizi
Zotama Dzina lomweli
La Yesu, ndiwoonayo
Wopatsa dalo lonseli
Ndilakalaka Iyeyu
Wofera ine pansitu;
Pakuda nkhaŵa ine bii
Nditchula Dzina lomweli,
Pakuda nkhaŵa ine bii
Nditchula Dzina lomweli.

Zokoma etu nthaŵizi
Ndicheza naye Mlungudi;
Koma kwathu m’Mwambamo
Kumwona ndi koposako.
Pobvula ine thupili,
Ndiloŵa Dziko lakedi;
Ndidzati nthaŵi yomweyo;
“Tsalani bwino pansipo.”
Ndidzati nthaŵi yomweyo;
“Tsalani bwino pansipo.”

Exit mobile version