Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 331 NDILI ndi kwathu ine,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 331 NDILI ndi kwathu ine,

 

NDILI ndi kwathu ine,
Kumwamba kowalako;
Komwe angelo ayimba,
Ndili ndi kwathu ine.

(M) Kosamangika ndi manja,
(O) Ndi manja,
(M) Kwathu
(O) Kwathuko,
(M) Kokongolako
(O) Kokongolako,
Komwe angelo ayimba
Ndili ndi kwathu ine.

Ndili ndi kwathu ine,
Kumene ndikakhale;
Komwe angelo ayimba,
Ndili ndi kwathu ine.

Ndili ndi kwathu ine,
Kosasinthika konse;
Komwe angelo ayimba,
Ndili ndi kwathu ine.

Exit mobile version