Chichewa Christian Hymns
Hymn 327 NTCHITO yonse yakeyo
NTCHITO yonse yakeyo
Yatha m’dzikoli linoli
Mlendo wafikatuko
Pokocheza leroli.
’Tate, mwakusunga kwanu
Timusiya mwana wanu.
’Tate, mwa kusunga kwanu
Timusiya mwana wanu.
Yathatu misoziyo
Zobisika zonse mbee!
Aweruza bwinoko
Ndiye Wolungamayo.
Komwe Mbusa kwawoko
Atengera nkhosa zonse,
Zake asungiramo
Zosaopa kanthu konse.
Onse akulapawo
Ayang’ana mtanda wake;
Aphunzira komweko
Zonse za kukonda kwake.
Dothili kudothilo,
Pfumbili kupfumbi tere;
Mpaka adzadzukanso
Timusiya mumtendere.
