Chichewa Christian Hymns
Hymn 326 TSIKU Iidzafika mbale,
TSIKU Iidzafika mbale,
Limene udzafa;
Udzatani pamaso pa,
Mfumu ya mafumu,
Siya zoipa zako,
Tsamira pa Yesu;
Zedi anafera iwe-e!
Kuti upulumuke.
Mnyamata gwiritsa Yesu,
Mtsikana bwerera;
Kuti wina angalande,
Korona wa moyo.
