Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 325 KODI uli ndi chisoni

Chichewa Christian Hymns

Hymn 325 KODI uli ndi chisoni

 

KODI uli ndi chisoni
Choliritsa mtima wako?
Kweza maso, ndi Atate
Akumvetsa zonsezi.

Kodi umadandaula;
“Mbale wanga waferanji?”
Kumbukira Wakumtenga
Saphophonya konse ’yi.

Mbale wako unamkonda,
Koma Yesu amkondetsa;
Anamfuna nagomtenga;
Usammane Yesu’yi

Pakutsazikana nanu
Ndi potseka maso ake,
Imfa, bii! Anangogona
Koma adzadzukanso.

Usalire; Mpulumutsi
Analaŵa imfa Yekha;
Imfa yomwe nagonjetsa
Potuluka m’mandamo.

Chikondano sichifera;
Mbale wako udzamwona
Kwathu komwe; zipirira
Mpaka ukafikako.

Leroli chisoni chokha,
Tsiku lija kungokondwa;
Kweza maso osalira,
Yesu akukondadi.

Exit mobile version