Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 280 YESU, afuna iwe unke kwawoko,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 280 YESU, afuna iwe unke kwawoko,

 

YESU, afuna iwe unke kwawoko,
Loŵa m’njira yake yakuyerayeratu;
Anadzera m’Mwamba kutiperekezako;
Yamba msanga iwe kunka kwanuko.

Tsata, tsata, nditsatadi Yesu;
Iwetu, iwetu, ukatsatanso.
Tsata, tsata, nditsatadi Yesu;
Inu nonse mukatsate Mbuyeyo

Ngati umtsata Mpulumutsi wakoyo,
Udzakhaliranso kuli Mbuye wakoyo;
Adzapulumutsa thupi, mzimu wakonso,
M’mphamvu ndi chilango cha zoipazo.

Kunsi kudambo, pena m’mwamba m’phirimo,
Pomwe pali Yesu ndidzayenda yendapo:
Andiperekeza bwino m’njira yakeyo,
Kuli Mzinda wa Mulungu wangayo.

Exit mobile version