Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 275 NTHAWI yathu yafikatu,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 275 NTHAWI yathu yafikatu,

 

NTHAWI yathu yafikatu,
Yoti tikagwire ntchito;
Monga Yesu ananena,
Panyanja ya Galileya.

Tikankhiretu kwakuya,
Ngakhale kuli zoopsa;
Ngakhale mafunde ali olimba,
Tidzapitabe mtsogolo.

Yesu anawauzatu,
Panyanja ya Galileya;
“Lero ndikusandutsani,
Kuti mudzasodze anthu.”

Ngakhale kuli mavuto,
Yesu ali kuyitana;
Mwa Iye tidzalimbika,
Ndipo tidzakhala naye.

Exit mobile version