Chichewa Christian Hymns
Hymn 270 NDILIRA mtima wotamanda
NDILIRA mtima wotamanda
Mlungu, ndi woyera,
E, mtima woyamika mwazi
Munandikhetsera.
Mtimatu wopirira ndi
Wofatsa mkati mwake,
Mumveka Mbuye Yesu yekha,
Ndiye Mfumu yake.
Ndilira mtima wakulapa
Ndi womvera Yesu,
Wosasiyana ndi Ambuye
Wakukhala m’mwemo.
E, mtima watsopano ndi
Wodzala ndi chikondi,
Wangwiro ndi wokoma, Mbuye,
Wonga wanu wonse.
Mkhalidwe wanu mundipatse
Ndifanane nanu
Mulembe m’mtima mwanga Dzina
La chikondi chanu.
