Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 269 NDILIRA ine kukayenda

Chichewa Christian Hymns

Hymn 269 NDILIRA ine kukayenda

 

NDILIRA ine kukayenda
M’njira ndi Mulungu;
Ndilira nyali ndikaone
Njira Ya kwa Yesu.

Chimwemwe chija chamumtima
Ndinalaŵa kale
Poyambutsata ine Yesu,
Chili kuti tere?

Kalelo m’mtima ndinakondwa,
Tere ndingolira,
Zokoma zonse zapadziko
Sizindikwanira.

Mubwere, Mzimu wa mpumulo,
Mundileze m’kati;
Ndidana nazo zoipazo
Zinakuchotsani.

Mundichotsere tchimo lonse
Ndinakonda kale,
E, muligwetse kuti ndinu
Mfumu mukakhale.

Mkatero ndidzayenda m’njira
Ndi Mulungu wanga,
Idzandiunikira nyali
Njira ya Kumwamba.

Exit mobile version