Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 268 POKHALA mtendere mu mtimangamu,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 268 POKHALA mtendere mu mtimangamu,

 

POKHALA mtendere mu mtimangamu,
Pamene ndisaukanso,
Pamene mabvuto ndi akuludi,Moyo wangawu ngwabwinotu.

Moyowu, ngwabwino,
Moyo wanga ulitu bwino.

Ngakhale Satana andizunza ’ne,
Chilipo chitonthozacho;
Chifundo cha Kristu anafera ’ne,
Kundipatsa ’ne moyo wake.

Uchimo unapachikidwa pomwe
Pamtanda wa Yesu Mbuye;
Machimo angawo anatherapo;
Mbuye wanga, ndiyamika ’Nu.

Ambuyathu, ndikhumba tsiku lija
Limene ndidzaona ’Nu;
Lipenga limveke, ndidzakondwatu
Pakukomana ndi Yesuyo.

Exit mobile version