Chichewa Christian Hymns
Hymn 263 AMBUYE mundisunge
AMBUYE mundisunge
Pafupi ndinutu;
Palibe malo pena
Popuma pansipa.
Adani andizinga,
Zoipa m’katimo;
Chifundo chanu Yesu
Chikonze m’mtimamo.
Ndikabisala mwanu
Ndilibe mantha ’yi;
Ndikasungidwa kwanu
Mumtima muti phee!
Ndi mphamvu yanu yokha
Ndiposa ’daniwo;
Chifundo chanu Mbuye
Chitchinjirize ’ne
Ndidzaonana nanu
Mokondwakondwadi.
Oyera mtima onse
Apenya Mbuyeyo.
Kumwamba n’dzaimbira
Kukoma kwanuku;
N’dzatama nthaŵi zonse
Chikondi chanucho.
