Chichewa Christian Hymns
Hymn 260 ODALA ndi onsewo,
ODALA ndi onsewo,
Overa m’mtima mwawo;
Adzawonana ndi Mulungu,
Yesu ndiye wawo.
Ambuye anachoka,
Kumwamba, mwini moyo;
Wofatsa anakhala nafe,
Mfumu ya chisomo.
Mu mtima wakufatsa,
Akonda kukhalabe;
Asankha mtima wakuyera,
Ndiwo nyumba yake.
Tifuna Inu, Mbuye,
M’tininkhe mtima uwu;
Wodzichepetsa, wakuyera.
Woyenera Inu.
