Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 26 NDIKULEMEKEZA

Chichewa Christian Hymns

Hymn 26 NDIKULEMEKEZA

 

NDIKULEMEKEZA
Ambuye Mpulumutsi wanga;
Moyo ndi mtima wanga
ndilikukondwa mwa Mulungu.

Ndiye anayang’ana
umphaŵi wa mdzakazi wake;
Onse adzandiyesa ine wodala nsiku zonse.

Ndiye wamphamvu zonse anandichitira zazikulu;
Dzina la Ambuyanga lili loyera kopambana.

Ndiye amachitira chifundo anthu a mibadwo,
E! a mibadwo yonse yakumuopa ndi kummvera.

Iye amazichita zamphamvu nawo mkono wake;
Iye nabalalitsa omwe anyada nadzitama

Iye natsitsa kunsi mafumu ku mipando yawo.
Iye nakweza konko omwe afatsa nasauka.

Ife amakhutitsa anjala ndi zabwino zake,
Ndi olemera onse naŵaingits’ opanda kanthu.

Monga anapangana ponena kwa makolo athu,
Ali kuthandizadi lero anake a Yakobo,

Poti akumbukira atate wathu Abrahamu;
Inde chifundo chokha akuchitira ana ake.

Exit mobile version