Chichewa Christian Hymns
Hymn 254 PAMENE ndisawuka,
PAMENE ndisawuka,
Pamene ndivutidwa;
Mizimu yakuipa,
Ikadza nindiyesa.
Mulungu wanga,
Mwini mphamvu;
M’kandikumbukire ‘ne.
Pamene ndilemedwa,
Ndi zakuipa zanga;
Polowa mdima m’mtima,
Pochita ine mantha.
Masiku anga onse,
Mulungu mundisunge;
Pamene ndimwalira,
Ndi tsiku lomaliza.
