Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 248 M’MENE ine ndisauka

Chichewa Christian Hymns

Hymn 248 M’MENE ine ndisauka

 

M’MENE ine ndisauka
Ndi zoipa zangazo,
Ndidzapita kwa Mulungu,
Adzandilandiratu.

Mlungu adzandilandira,
Iye ndiye ’Tate wanga;
Watumiza Mwana wake
Andifere kalelo.

Ngatitu abwenzi anga
Sandikonda ine ’yi,
Ndikhulupirire Mlungu,
Iye sandikana ’yi.

Pansi pano ndili mlendo,
Kwathu ndi Kumwambako;
M’mene ndimalira ine
Ndidzapita komweko.

Exit mobile version