Chichewa Christian Hymns
Hymn 241 MTENDERE uli m’mtima mwathumu,
MTENDERE uli m’mtima mwathumu,
Chifukwa mwazi watitsuka mbuu!
Zakutsogolo sitidziŵa’yi;
Adziŵa Yesu wathu zonsezi.
Abale angakhale m’talimo
Mbuyethu asungira onsewo.
Imfa ndi manda sitiopa ’yi,
Chifukwa Yesu wazithetsadi.
Mtendere wopambana m’Mwambamo
Pakufa ife tidzaonanso.
