Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 237 SINDINANYENGEDWA konse

Chichewa Christian Hymns

Hymn 237 SINDINANYENGEDWA konse

 

SINDINANYENGEDWA konse
Pakutsata Yesuyo;
Yesu apambana zonse
Ndinalingalirazo.
Pakuyenderana naye
Ndimamdziŵa ndi woona;
Ndifunitsa anthu onse Adziŵenso Yesuyo!
Ndifunitsa anthu onse Adziŵenso Yesuyo!

Sindinanyengedwa konse:
Yesu wachotsera phe!
Zakuchimwa zanga zonse
Zakupsinja mtimazo.
Yesu potsagana nane
Wandidzaza ndi mtendere;
Kundisunga, kundikonda
Sadzaleka konse ’yi!
Kundisunga, kundikonda,
Sadzaleka konse ’yi!

Sindinanyengedwa konse,
Yesu adzabwerabe;
Mtima wanga undiuza
Akuyandikiradi
Omwe sangamzindikire
Andinyoza nandijeda,
Koma Yesu ati zedi;
“Ine ndidzabweradi.”
Koma Yesu ati zedi;
“Ine ndidzabweradi.”

Sandinyenga, salephera;
Yesu wadalitse ’ne
Mpulumutsi ndi Myeretsi
Ndi Mchiritsi yemweyo
Wandiyanjanitsa naye,
Mtima wanga nakhutitsa;
Sindinanyengedwa konse,
Yesu akwaniradi!
Sindinanyengedwa konse,
Yesu akwaniradi!

Exit mobile version