Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 234 IMFA ndi mfumu ya mdimawo,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 234 IMFA ndi mfumu ya mdimawo,

 

IMFA ndi mfumu ya mdimawo,
Anthu oipa imangawo,
Akhristu amapulumuka.
Omwe aimbira moyo,
Moyo ndi moyo ndi moyo,
Wosalekana ndi moyo
Wosamaliza Mulunguyo.

Yesu anafa pamtandapo,
Mzimu woipa nugomapo,
Ndi ife titame Mulungu.
Ndife tamasudwa m’moyo
Imfa ithedwa ndi moyo,
Tsiku lomaliza moyo
Wosamaliza Kumwambako.

M’mitima mwathu mwakhala mbee!
Mtambo wamdima wang’ambwa ke!
Panyanjapo pagawanika.
Ndife tipita ku moyo,
Mtima wabwino ndi moyo;
Kumbanda kucha kwa moyo
Kumatiuza za dzuŵalo.

Akumangidwa ndi mzimuwo,
Mudze ndi ife kwa Yesuko,
Akuchotsereni magoli,
Nadzakupatsani moyo,
Mlandu walipa ndi moyo,
Moyo ndi moyo ndi moyo,
Tambirana za moyowo.

Exit mobile version