Chichewa Christian Hymns
Hymn 229 POYAMBAPO ndakondwadi.
POYAMBAPO ndakondwadi.
N’tapeza Inu Mbuyetu;
Ndiimba nyimbo yomweyi,
Kukondwa sindikhala duu!
Kalero! Kalero!
Wandisambitsa m’mtimamo;
Wandiweruza lomwelo,
Kupempha ndi kukondwako.
Kalero! Kalero!
Wandisambitsa m’mtimamo.
Mnyamata wake ndinetu,
Ndimvera mawu akewo;
Ndam’patsa mtima wonsewu,
Ndim’tumikire pansipa.
Kumwamba ndidzanenadi,
Zachipangano chathucho;
Wamoyo sindim’siya ‘yi,
Nditafa ndinka kwawoko.
