Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 219 YESU Mbuyetu, mwafera

Chichewa Christian Hymns

Hymn 219 YESU Mbuyetu, mwafera

 

YESU Mbuyetu, mwafera
Mphulupulutu zanga,
Ndimo ndamva mund’itana,
Mutitu, Msachedwa.

Zonse za m’dziko zidzatha,
Koma za moyo m’Mwamba
Zomwe zidzakhalitsatu,
Chakatu ndi chaka.

Nyengo ifika, chenjera!
Adzakukana m’Mwamba.
Lapa zoipa zakozo,
Kuti ukaloŵe.

Exit mobile version