Chichewa Christian Hymns
Hymn 211 TIDZALAKALAKA kuwonana naye,
TIDZALAKALAKA kuwonana naye,
Monga Zakeyu anawonana naye;
Tidzalakalaka kuwonana naye,
Mwana wa Mulunguyo.
(Tidzalakalaka) kuwonana naye,
(Tidzalakalaka) kuwonana naye;
(Tidzalakalaka) kuwonana,
Naye, naye, Mbuye.
Ngatitu tifuna kuwonana naye,
Tingomupatsatu mitima yathuyi;
Adzatipatsatu moyo wosathawo,
Moyo wamuyayawo.
Tiyeni tipereke mitima yathu,
Kwa Ambuye wathuyo wa Kumwambako;
Adzatipatsatu moyo wosathawo,
Moyo wamuyayawo.
