Chichewa Christian Hymns
Hymn 198 CHITSIMECHO cha mwaziwo
CHITSIMECHO cha mwaziwo
Udzera mwa Mbuyanga;
Wochimwa ndikasambamo,
Nditaya tchimo langa.
Wakuba uja nachiona,
Nangokhulupira,
Ambuye namva pempholo,
M’Mwambamo namlandira.
Ambuye, mwazi wanuwo
Siitha mphamvu yake,
E, Mpingo wonsewo
Wayera m’kati mwake.
Chionerere mwaziwo
Wofuma m’bala lanu,
Sindinaleke ineyo
Kutama mtima wanu.
Kumwamba komwe n’dzaimbira
Mpulumutsi wanga,
Chifukwa ayeneratu,
Wakonza m’mtima mwanga.
