Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 186 MVERANI mbiri yozizwitsa

Chichewa Christian Hymns

Hymn 186 MVERANI mbiri yozizwitsa

 

MVERANI mbiri yozizwitsa
Ya Yesuyo kalelo;
Iyeyo ’nadza pansi pano
Kutipulumutsa ’fe.

Ndani anatiwombola?
Mwana wa Mlungu pa mtanda.
Anatani?
Anafera.
Ali kuti?
Akhaladi m’Mwamba kutipempherera.

Palibe m’modzi akanatha
Kuloŵa m’malo mwake;
Ngakhale anali wamkulu
’Nasiyidwa namnyoza.

Kodi mudzampembedza Mbuye
Mpulumutsi wathuyo?
Kodi inu mudzaloŵamo
Mu Ufumu wakewo?

Exit mobile version