Chichewa Christian Hymns
Hymn 183 MUDZE kwa Yesu, musachedwe.
MUDZE kwa Yesu, musachedwe.
Kalata ilozera njira;
Amaitanatu tonsefe,
Bvomerani Iye.
Tidzakondweradi m’Mwambamo
Posonkhana komwe kuli ’Ye;
Tidzakhala naye komweko
Ku Dziko losafa.
Lolani ana, mumve Mlungu,
Tsegulani mitima yanu,
Sankhani Iye, Bwenzi lanu;
Musachedwe, mudze.
Ganizansoni, ali pano,
Mthenga wake mverani lero;
Mawu okoma ati lero,
Musachedwe, mudze.
