Chichewa Christian Hymns
Hymn 180 MALO alimo m’nyumba ya Yesu,
MALO alimo m’nyumba ya Yesu,
Ndi nyimbo zake zakuitana:
“Loŵa, loŵa,
Tsopano loŵatu.”
Mdima ufika, dzuŵa laloŵa,
Nthunzi zilipo, wadza usiku.
Nyumba yodyera ilikudzaza;
Idza nuloŵe, Mkwati anena:
Chakudya ichi ndi cha iwenso,
Madzi amoyo umwe kolere.
Onse am’Mwamba ali momwemo,
Ndipo angelo akuitana:
Mawu a Yesu ati: “Msangatu
Idza, wochedwa, loŵa m’nyumbamo.”
Msanga adzachitseka chitseko,
Adzakuuza: “Choka, chokatu.”
Choka,choka,
Anena chokatu.
