Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 18 POKHALA Inu

Chichewa Christian Hymns

Hymn 18 POKHALA Inu

 

POKHALA Inu
mpotikonda ndithu,
Yehova Wamakamu
Moyo wanga; ulakalaka Inu,
Ukomokanso ndikufuna,
Mabwalo a Yehova.
Mtima wanga ndi thupi langa,
Zifuulira kwa Mulungu wa moyo.

Odala iwotu akugonera,
M’nyumba mwanu Yehova;
Nthawi zonse akulemekezani,
Odala munthu yemwe,
Mphamvu yake ili mwa Inu;
Mu mtima mwake ndi moyera
Mulitu makhwalala a ku Zioni.

Exit mobile version