Chichewa Christian Hymns
Hymn 164 WANENA ndi Yesu,
WANENA ndi Yesu,
Mawu onse awa;
Mfumu yamtendere,
Yalonjeza kuti:
“Sindim’tulutsa
sindidzam ‘taya;
Wakudza kwa Ine
Sindim’tulutsa,
sindidzam’taya
Wakudza kwa Ine.”
“Mfulu ndi kapolo,
Adzetu kwa Ine;”
Wanena ndi Yesu,
Mawu onse awa.
Onse akulapa,
Adzawona mwayi;
Ndipo adzayimba,
Pamodzi ndi Yesu.
