Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 153 NDAKUMANA ndi bwenzi lokomalo,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 153 NDAKUMANA ndi bwenzi lokomalo,

 

NDAKUMANA ndi bwenzi lokomalo,
Ndiye Yesu mtetezi wanga;
Ndayang’ana, palibe wina padziko.

M’mtima mwanga mualowa chisangalalo,
Popeza ndawomboledwa;
(Chinanso) ndalandira
Mzimu Woyera (zedi)
Moyo wanga wawomboledwa

Ndasamba m’mwazi wa chitsime chake,
Cha Ambuye mtetezi wanga;
Ndayang’ana, palibe wina padziko.

Ndayera ndi mwazi wa Ambuyeyo,
Ndine wake wa Ambuyewo;
Ndayang’ana, palibe wina padziko.

Exit mobile version