Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 15 YEHOVA ndiye Mbusa wanga,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 15 YEHOVA ndiye Mbusa wanga,

 

YEHOVA ndiye Mbusa wanga,
sin’ngasoŵe konse;
Andigonetsa pali busa
La misipu yonse.

(Ndiye Mbusa wanga,
Ndiye Mbusa wanga!
Yehova ndiye Mbusa wanga,
Sin’ngasoŵe konse)

Kumadzi kuli njiratu,
Andiyendetsa bwino,
Nalimbikitsa moyo wanga,
Ndi chifundo chino.

Pabande lolunjika,
Andilondolera njira,
Chifukwacho cha dzina lake,
Anandisungira.

Chigwa choopsacho cha imfa,
Ndikachiloŵera;
Ndilibe mantha, muli ndi’ne,
Ndodo ndiigwira.

Pamaso pa adaniwo,
Mwayala gome langa;
E, mutu mwaudzoza,
Chisefuka chikho changa.

Zabwino ndi zokoma,
zinditsata chitsatire;
E, m’nyumba ya Yehova,
Ndidzakhala chikhalire.

Exit mobile version