Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 146 KODI ulikulemedwa

Chichewa Christian Hymns

Hymn 146 KODI ulikulemedwa

 

KODI ulikulemedwa
Ndi zoipazo?
Idza kuno, ati Yesu,
Pumako.

Ndikamzindikira ninji
Mbuye wangayo?
Ali ndi mabala m’manja
Mwakemo.

Kodi ali ndi chilemba
M’phumi mwakemo?
E, chilembacho chaminga
Chilimo.

Ndikampeza, ndikamtsata
Ninji pansipa?
Masauko ndi misozi
Zilipo.

Ndikamfunafuna Iye,
Ndipezenjiko?
Kumaliza kwa chisoni
Chonsecho.

Ndikampempha anditenge,
Akataniko?
Ati Yesu, “Idza msanga,
Idzatu.

Exit mobile version