Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 137 UTHENGA wa Ambuye

Chichewa Christian Hymns

Hymn 137 UTHENGA wa Ambuye

 

UTHENGA wa Ambuye
Aleluya.
Uthenga ndipereka kwa Inu;
Walembedwa
M’mawu ake
Aleluya,
Werengani m’khale ndi moyo.

(M) Yang’ana,
(O) Yang’ana mbale wanga,
(Yang’ana)
Kuti upulumuke:
Walembedwa m’Mawu ake
Aleluya,
Yang’ana ukhale ndi moyo.

Uthenga ngwachikondi
Aleluya,
Uthenga’wu abale ndi wanu;
Ndi Uthenga wa Kumwamba
Aleluya,
Yesu ndiye anena zedi.

Moyo wa Yesu mbale
Aleluya,
Moyowo wa Ambuyeyo ngosatha:
Ungoyang’ana kwa Yesu
Aleluya,
Yang’ana ukhale ndi moyo.

Exit mobile version