Chichewa Christian Hymns
Hymn 1 NDINU wakuyera! Wamphamvu zonse.
NDINU wakuyera! Wamphamvu zonse.
Nthaŵi ya m’mamaŵayi tiimba nyimboyi.
Mlengi wachifundo, tikuyamikani,
E! Mlungu Mmodzi mwa Atatuwo.
Ndinu Wakuyera! Anthu ochuluka
Akuimbirani, nakupempharanibe;
Akumwamba omwe nagwadira Inu,
Wachikhalire ndi wosafa ’yi.
Ndinu wakuyera!
Ife akuchimwa
Zaulemerero zanu sitiona’yi;
Mwayera nokha, wina saoneka
Wangwiro m’mphamvu ndi m’kuyeramo.
Ndinu wakuyera! Zakumwamba zonse
Ndi zapansi zitamabe dzina lanulo;
Mlengi wachifundo,
Mphambi,
Ambuyathu,
E! Mlungu Mmodzi mwa Atatuwo.
