Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 613 Dziko lonse nla Mulungu

Chichewa Believers Christian Hymns

Hymn 613 Dziko lonse nla Mulungu

 

Dziko lonse nla Mulungu

Kuti limbalire dzinthu;

M’munda zonse zimamera

Zakukoma ndi zoipa;

Mmera udza, bwino ngala,

Maso omwe amakwima;

Mutilole, Mwini dzinthu,

Tikakhale dzinthu zanu.

Exit mobile version